Isaiah 10:13 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pakuti mfumuyo ikuti, “Ndachita zimenezi ndi mphamvu zanga ndiponso ndi nzeru zanga, pakuti kumvetsa nkwanga. Ndachotsa malire a mitundu ya anthu, ndipo ndafunkha chuma chao. Ndaŵatsitsa amene anali pa mipando yaufumu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Popeza anati, Mwa mphamvu ya dzanja langa ndachita ichi, ndi mwa nzeru yanga; pakuti ine ndili wochenjera; ndachotsa malekezero a anthu, ndalanda chuma chao, ndagwetsa monga munthu wolimba mtima iwo okhala pa mipando yachifumu;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pakuti mfumuyo ikuti, “ ‘Ndachita zimenezi ndi dzanja langa, ndiponso ndi nzeru zanga, chifukwa ndine wozindikira zinthu. Ndinachotsa malire a mitundu ya anthu, ndinafunkha chuma chawo; ndinagonjetsa mafumu awo monga munthu wamphamvu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Popeza anati, Mwa mphamvu ya dzanja langa ndacita ici, ndi mwa nzeru yanga; pakuti ine ndiri wocenjera; ndacotsa malekezero a anthu, ndalanda cuma cao, ndagwetsa monga munthu wolimba mtima iwo okhala pa mipando yacifumu;