Isaiah 10:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Dzanja langa lagwira chuma cha mitundu ya anthu, monga momwe munthu amagwirira chisa cha mbalame. Monga momwe anthu amatolera mazira osiyidwa, ndimo m'mene Ine ndidasonkhanitsira dziko lonse lapansi. Ndipo panalibe mbalame ndi imodzi yomwe yoti mapiko phephere-phephere, kapena yoti kukamwa yasa kapena yolira kuti psepsepse.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
dzanja langa lapeza monga chisa, chuma cha mitundu ya anthu, ndipo monga munthu asonkhanitsa dziko lonse lapansi, ndipo panalibe chogwedeza phiko, kapena chotsegula pakamwa, kapena cholira pyepye.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Dzanja langa lagwira chuma cha mitundu ya anthu ngati momwe munthu amagwirira chisa cha mbalame, ngati momwe anthu amatolera mazira osiyidwa, motero inenso ndinasonkhanitsa mayiko onse; palibe mbalame imene inakupiza mapiko ake, kapena kuyasama kukamwa kuti ilire.’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
dzanja langa lapeza monga cisa, cuma ca mitundu ya anthu, ndipo monga munthu asonkhanitsa mazira osiyidwa, ine ndasonkhanitsa dziko lonse lapansi, ndipo panalibe cogwedeza phiko, kapena cotsegula pakamwa, kapena colira pyepye.