Isaiah 10:15 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Chauta akuti: “Kodi nkhwangwa ingathe kudzikuza kupambana munthu woigwiritsa ntchito? Kodi sowo ingathe kudzikuza kupambana munthu woigwiritsa ntchito? Ndiye kukhala ngati kuti mkwapulo ukuzunguza munthu, kapena ndodo yanyamula munthu!”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kodi nkhwangwa idzadzikweza yokha, pa iye amene adula nayo? Kodi chochekera chidzadzikweza chokha pa iye amene achigwedeza, ngati chibonga ingamgwedeze iye amene ainyamula, ngati ndodo inganyamule kanthu popeza ili mtengo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kodi nkhwangwa ingathe kudzikuza kupambana woyigwiritsa ntchito, kapena macheka angathe kudzikuza kupambana wowagwiritsa ntchito? Ndiye kukhala ngati kuti chikwapu chikuzunguza munthu amene wachinyamula, kapena ngati kuti ndodo ikuopseza amene wayinyamula!
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kodi nkhwangwa idzadzikweza yokha, pa iye amene adula nayo? kodi cocekera cidzadzikweza cokha pa iye amene acigwedeza, ngati cibonga ingamgwedeze iye amene ainyamula, ngati ndodo inganyamule kanthu popeza iri mtengo.