Isaiah 10:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nchifukwa chake Ambuye, Chauta Wamphamvuzonse, adzatumiza matenda oondetsa kwa ankhondo amphamvu a mfumu ya ku Asiriya. Ndipo mfumuyo kunyada kwake kudzapsa ndi moto wosazimika.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake Ambuye, Yehova wa makamu, adzatumiza kuonda mwa onenepa ake; ndipo pansi pa ulemerero wake padzayaka kutentha, konga ngati kutentha kwa moto.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nʼchifukwa chake Ambuye Yehova Wamphamvuzonse adzatumiza matenda owondetsa kwa ankhondo amphamvu; kunyada kwa mfumuyo kudzapsa ndi moto wosazima.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace Ambuye, Yehova wa makamu, adzarumiza kuonda mwa onenepa ace; ndipo pansi pa ulemerero wace padzayaka kutentha, konga ngati kutentha kwa moto.