Isaiah 10:17 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mulungu, Kuŵala kwa Israele, adzakhala ngati moto. Mulungu, Woyera Uja wa Israele, adzakhala ngati malaŵi a moto. Motowo udzaŵatentha ndi kuŵapsereza ngati minga ndi mkandankhuku pa tsiku limodzi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kuwala kwa Israele kudzakhala moto, ndi Woyera wake adzakhala lawi; ndipo lidzatentha ndi kuthetsa minga yake ndi lunguzi wake tsiku limodzi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mulungu, Kuwala kwa Israeli, adzakhala ngati moto, Woyera uja wa Israeli adzakhala ngati malawi a moto. Motowo udzawatentha ndi kuwapsereza ngati minga ndi mkandankhuku pa tsiku limodzi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kuwala kwa Israyeli kudzakhala moto, ndi Woyera wace adzakhala lawi; ndipo lidzatentha ndi kuthetsa minga yace ndi lunguzi wace tsiku limodzi.