Isaiah 10:2 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pakutero amapotoza malamulo poweruza amphaŵi mosalungama. Amaŵalanda zoŵayenerera anthu anga osauka, amafunkha za akazi amasiye ndi kubera ana amasiye!
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
kuwapatulira osowa kuchiweruziro, ndi kuchotsera anthu anga aumphawi zoyenera zao, kuti alande za akazi amasiye, nafunkhire ana amasiye!
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
kuwalanda anthu osauka ufulu wawo ndi kumana chilungamo osautsidwa pakati pa anthu anga, amalanda zinthu za akazi amasiye ndi kubera ana amasiye.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
kuwapatulira osowa kuciweruziro, ndi kucotsera anthu anga aumphawi zoyenera zao, kuti alande za akazi amasiye, nafunkhire ana amasiye!