Isaiah 10:20 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsiku limenelo otsalira a ku Israele, opulumuka a m'banja la Yakobe, sadzadaliranso anthu amene adaŵakantha, koma ndithu adzadalira Chauta, Woyera Uja wa Israele.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo padzakhala tsiku lomwelo, kuti otsala a Israele, ndi iwo amene anapulumuka a nyumba ya Yakobo, sadzatsamiranso iye amene anawamenya; koma adzatsamira Yehova Woyera wa Israele, ntheradi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsiku limenelo otsalira a ku Israeli, opulumuka a nyumba ya Yakobo, sadzadaliranso anthu amene anawakantha, koma adzadalira Yehova, Woyerayo wa Israeli.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo padzakhala tsiku lomwelo, kuti otsala a Israyeli, ndi iwo amene anapulumuka a nyumba ya Yakobo, sadzatsamiranso iye amene anawamenya; koma adzatsamira Yehova Woyera wa Israyeli, ntheradi.