Isaiah 10:24 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nchifukwa chake Ambuye, Chauta Wamphamvuzonse, akunena kuti, “Inu anthu anga okhala ku Ziyoni, musaŵaope Aasiriya pamene akukanthani ndi ndodo, nakumenyani ndi zibonga zao, monga m'mene Aejipito ankachitira.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake atero Ambuye Yehova wa makamu, Inu anthu anga okhala m'Ziyoni, musaope Asiriya; ngakhale amenya inu ndi chibonga, kapena kukusamulira iwe ndodo yake, monga amachitira Ejipito.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nʼchifukwa chake, Ambuye Yehova Wamphamvuzonse akunena kuti, “Inu anthu anga okhala mu Ziyoni, musawaope Asiriya, amene amakukanthani ndi ndodo nakumenyani ndi zibonga monga mmene Igupto anachitira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace atero Ambuye; Yehova wa makamu, Inu anthu anga okhala m'Ziyoni, musaope Asuri; ngakhale amenya inu ndi cibonga, kapena kukusamulira iwe ndodo yace, monga amacitira Aigupto.