Isaiah 10:26 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ine, Chauta Wamphamvuzonse, ndidzaŵakwapula monga momwe ndidakwapulira Amidiyani ku thanthwe la Orebu. Ndi ndodo yanga ndidzaŵalanga, monga momwe ndidalangira Aejipito panyanja paja.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yehova wa makamu adzamuutsira chikoti, monga m'kuphedwa kwa Midiyani pa thanthwe la Orebu; ndipo chibonga chake chidzakhala pamwamba pa nyanja, ndipo adzaisamula monga anachitira Ejipito,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova Wamphamvuzonse adzawakwapula ndi chikwapu, monga momwe anakwapulira Amidiyani ku thanthwe la Orebu; ndipo adzatukula ndodo yake pa madzi ndikuwalanga monga analangira Igupto pa nyanja.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yehova wa makamu adzamuutsira cikoti, monga m'kuphedwa kwa Midyani pa thanthwe la Orebu; ndipo cibonga cace cidzakhala pamwamba pa nyanja, ndipo adzaisamula monga anacitira Aigupto,