Isaiah 10:27 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsiku limenelo ndidzakusanjulani katundu wa Aasiriya pa mapewa anu, ndi goli lao m'khosi mwanu, golilo lidzathyoka chifukwa cha kunenepa.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo padzakhala tsiku lomwelo, kuti katundu wake adzachoka pa phewa lako, ndi goli lake pakhosi pako; ndipo goli lidzathedwa chifukwa cha kudzoza mafuta.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsiku limenelo katundu wawo adzachotsedwa pa mapewa anu, goli lawo lidzachoka mʼkhosi mwanu; golilo lidzathyoka chifukwa cha kunenepa kwambiri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo padzakhala tsiku lomwelo, kuti katundu wace adzacoka pa phewa lako, ndi gori lace pakhosi pako; ndipo gori lidzathedwa cifukwa ca kudzoza mafuta.