Isaiah 10:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kodi mudzatani pa tsiku lachilango pofika namondwe wochokera kutali? Kodi mudzathaŵira kwa yani kuti akuthandizeni? Nanga chuma chanu mudzachisiya kuti?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mudzachita chiyani tsiku lakudza woyang'anira, ndi chipasuko chochokera kutali? Mudzathawira kwa yani kufuna kuthangatidwa? Mudzasiya kuti ulemerero wanu?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kodi mudzatani pa tsiku la chilango, pofika chiwonongeko chochokera kutali? Kodi mudzathawira kwa yani kuti akuthandizeni? Nanga chuma chanu mudzachisiya kuti?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mudzacita ciani tsiku lakudza woyang'anira, ndi cipasuko cocokera kutari? mudzathawira kwa yani kufuna kuthangatidwa? mudzasiya kuti ulemerero wanu?