Isaiah 10:34 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta adzaŵadula monga momwe anthu amadulira ndi nkhwangwa mitengo ya m'kati mwa nkhalango. Iwo adzagwa monga momwe imagwera ngakhale mitengo yaikulu ya ku Lebanoni.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo adzadula nkhalango za m'thengo ndi chitsulo, ndipo Lebanoni adzagwa ndi wamphamvu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova adzadula ndi nkhwangwa mitengo ya mʼnkhalango yowirira; Lebanoni adzagwa pamaso pa Wamphamvu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo adzadula nkhalango za m'thengo ndi citsulo, ndipo Lebano adzagwa ndi wamphamvu.