Isaiah 10:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kudzatsala nkungozyolika mwamanyazi pakati pa anthu ogwidwa kapena kufa pamodzi ndi ophedwa. Komabe mkwiyo wa Mulungu sudaŵachoke chifukwa cha zonsezi, ndipo mkono wake uli chisamulirecho kufuna kuŵalanga.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Adzangoweramira pansi pa andende, ndipo adzagwa pansi pa ophedwa. Mwa izi zonse mkwiyo wake sunachoke, koma dzanja lake lili chitambasulire.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kudzatsala nʼkungozolika mwamanyazi pakati pa anthu ogwidwa kapena kufa pamodzi ndi ophedwa. Komabe pa zonsezi mkwiyo wake sunawachokere, mkono wake uli chitambasulire.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Adzangoweramira pansi pa andende, ndipo adzagwa pansi pa ophedwa. Mwa izi zonse mkwiyo wace sunacoke, koma dzanja lace liri citambasulire.