Isaiah 10:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ine ndagonjetsa mizinda iyi: Kalino, Karikemisi, Hamati, Aripadi. Ndagonjetsanso Samariya ndi Damasiko.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kodi Kalino sali wonga ngati Karikemisi? Kodi Hamati sali ngati Aripadi? Kodi Samariya sali ngati Damasiko?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
‘Kodi Kalino sanagonjetsedwe monga Karikemesi? Kodi Hamati sali ngati Aripadi, nanga Samariya sali ngati Damasiko?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kodi Kalino sali wonga ngati Karikemesi? kodi Hamati sali ngati Aripadi? kodi Samariya sali ngati Damasiko?