Isaiah 11:10 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsiku limenelo mfumu yatsopano yochokera ku banja la Davide idzakhala chizindikiro kwa anthu a mitundu yonse. Onse adzasonkhana kwa iye, ndipo malo ake okhalapo adzakhala aulemerero.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo padzakhala tsiku lomwelo, kuti muzu wa Yese umene uima ngati mbendera ya mitundu ya anthu, amitundu adzafunafuna uwu; ndipo popuma pake padzakhala ulemerero.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsiku limenelo mfumu yatsopano yochokera pa Muzu wa Yese idzakhala ngati chizindikiro kwa anthu a mitundu yonse. Mitundu ya anthu idzasonkhana kwa Iye, ndipo malo awo okhalapo adzakhala aulemerero.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo padzakhala tsiku lomwelo, kuti muzu wa Jese umene uima ngati mbendera ya mitundu ya anthu, amitundu adzafunafuna uwu; ndipo popuma pace padzakhala ulemerero.