Isaiah 11:14 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Yuda ndi Efuremu adzathira nkhondo pa Afilisti kuzambwe, ndipo onsewo pamodzi adzalanda zinthu za anthu akuvuma. Adzalimbana ndi Aedomu ndi Amowabu, ndipo Aamoni adzaŵagonjera.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo adzagudukira mapewa a Afilisti kumadzulo; pamodzi adzafunkha ana a kum'mawa; adzatambasula dzanja lao pa Edomu ndi pa Mowabu; ndipo ana a Amoni adzawamvera.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yuda ndi Efereimu adzathira nkhondo pa Afilisti mbali ya kumadzulo; ndipo onsewo pamodzi adzalanda zinthu za anthu a kummawa. Adzalimbana ndi Edomu ndi Mowabu, ndipo Aamoni adzawagonjera.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo adzagudukira mapewa a Afilisti kumadzulo; pamodzi adzafunkha ana a kum'mawa; adzatambasula dzanja lao pa Edomu ndi pa Moabu; ndipo ana a Amoni adzawamvera.