Isaiah 11:15 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo Chauta adzaphwetsa kotheratu mwendo wa nyanja yofiira ya ku Ejipito. Adzatambalitsa dzanja lake ndipo adzaombetsa mphepo yotentha pa mtsinje wa Yufurate. Mtsinjewo udzagaŵikana m'timitsinje tisanu ndi tiŵiri, kuti anthu aoloke pouma.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yehova adzaononga ndithu bondo la nyanja ya Ejipito; ndipo ndi mphepo yake yopsereza adzagwedeza dzanja lake pa Mtsinje, ndipo adzaimenya ikhale mphaluka zisanu ndi ziwiri, nadzaolotsa anthu pansi pouma.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova adzaphwetsa mwendo wa nyanja ya Igupto; adzatambasula dzanja lake ndipo adzawombetsa mphepo yotentha pa mtsinje wa Yufurate. Iye adzawugawa mtsinjewo kukhala timitsinje tisanu ndi tiwiri kuti anthu athe kuwoloka powuma atavala nsapato.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yehova adzaononga ndithu bondo la nyanja ya Aigupto; ndipo ndi mphepo yace yopsereza adzagwedeza dzanja lace pa Nyanja, ndipo adzaimenya ikhale mphaluka zisanu ndi ziwiri, nadzaolotsa anthu pansi pouma.