Isaiah 11:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Padzakhala mseu waukulu woti ayendepo otsalira ku Asiriya aja, monga m'mene panaliri mseu waukulu woyendapo Aisraele pochoka ku Ejipito.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo padzakhala khwalala la anthu ake otsala ochokera ku Asiriya; monga lija la Israele tsiku lokwera iwo kutuluka m'dziko la Ejipito.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Padzakhala msewu waukulu woti ayendepo anthu ake otsalira amene anatsalira ku Asiriya, monga mmene panali msewu waukulu woyendapo Israeli pamene amachokera ku Igupto.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo padzakhala khwalala la anthu ace otsala ocokera ku Asuri; monga lija la Israyeli tsiku lokwera iwo kuturuka m'dziko la Aigupto.