Isaiah 11:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma amphaŵi adzaŵaweruza mwachilungamo, ndipo anthu otsika a pa dziko lapansi adzaŵagamulira mlandu wao mosakondera. Mau ochokera m'kamwa mwake adzakhala ngati ndodo yokanthira ochimwa, atalamula iyeyo anthu oipa adzaphedwa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
koma ndi chilungamo adzaweruza aumphawi, nadzadzudzulira ofatsa a m'dziko moongoka; ndipo adzamenya dziko lapansi ndi chibonga cha kukamwa kwake, nadzapha oipa ndi mpweya wa milomo yake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
koma amphawi adzawaweruza mwachilungamo, adzaweruza mwachilungamo mlandu wa anthu osauka a dziko lapansi. Iye adzakantha dziko lapansi ndi mawu ake; atalamula Iyeyu anthu oyipa adzaphedwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
koma ndi cilungamo adzaweruza aumphawi, nadzadzudzulira ofatsa a m'dziko moongoka; ndipo adzamenya dziko lapansi ndi cibonga ca kukamwa kwace, nadzapha oipa ndi mpweya wa milomo yace.