Isaiah 11:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mmbulu udzakhala pamodzi ndi mwanawankhosa, kambuku adzagona pansi pamodzi ndi mwanawambuzi, mwanawang'ombe ndi mwanawamkango adzadyera limodzi, mwana wamng'ono nkumaziŵeta zonsezo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mmbulu udzakhala pamodzi ndi mwanawankhosa, ndipo nyalugwe adzagona pansi ndi mwanawambuzi; ndipo mwanawang'ombe ndi mwana wa mkango ndi choweta chonenepa pamodzi; ndipo mwana wamng'ono adzazitsogolera.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mʼmbulu udzakhala pamodzi ndi mwana wankhosa, kambuku adzagona pansi pamodzi ndi mwana wambuzi, mwana wangʼombe ndi mwana wa mkango adzadyera limodzi ndipo mwana wamngʼono adzaziweta.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mmbulu udzakhala pamodzi ndi mwana wa nkhosa, ndipo nyalugwe adzagona pansi ndi mwana wa mbuzi; ndipo mwana wa ng'ombe ndi mwana wa mkango ndi coweta conenepa pamodzi; ndipo mwana wamng'ono adzazitsogolera.