Isaiah 13:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nyenyezi zonse zakumwamba sizidzaonetsanso kuŵala. Dzuŵa lidzada potuluka, ndipo mwezi sudzaŵala konse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa nyenyezi za kumwamba ndi makamu ao sizidzawala; dzuwa lidzada m'kutuluka kwake, ndipo mwezi sudzaonetsa kuwala kwake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nyenyezi zakumwamba ndiponso zonse zamlengalenga sizidzaonetsa kuwala kwawo. Dzuwa lidzada potuluka, ndipo mwezi sudzawala konse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa nyenyezi za kumwamba ndi makamu ao sizidzawala; dzuwa lidzada m'kuturuka kwace, ndipo mwezi sudzaonetsa kuwala kwace.