Isaiah 13:11 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta akuti, “Ndidzalanga anthu a dziko lapansi chifukwa cha kuipa kwao, ndidzalanga oipa chifukwa cha kuchimwa kwao. Ndidzathetsa kunyada kwa odzikuza ndipo ndidzatsitsa kudzitukumula kwa anthu ankhanza.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndidzalanga dziko lapansi, chifukwa cha kuipa kwao, ndi oipa chifukwa cha mphulupulu zao; ndipo ndidzaletsa kudzikuza kwa onyada, ndidzagwetsa kudzikweza kwa oopsa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndidzalanga dziko lonse chifukwa cha zolakwa zake, anthu oyipa ndidzawalanga chifukwa cha machimo awo. Ndidzathetsa kunyada kwa odzikuza, ndipo ndidzatsitsa kudzitukumula kwa anthu ankhanza.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndidzalanga dziko lapansi, cifukwa ca kuipa kwao, ndi oipa cifukwa ca mphulupulu zao; ndipo ndidzaletsa kudzikuza kwa onyada, ndidzagwetsa kudzikweza kwa oopsya.