Isaiah 13:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Choncho munthu aliyense adzabwerera kwa anthu akwao, aliyense adzathaŵira ku dziko lake, ngati mbaŵala zothaŵa anthu auzimba kapenanso ngati nkhosa zopanda wozikusa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo padzakhala kuti monga mbawala yothamangitsidwa, ndi monga nkhosa zosazisonkhanitsa anthu, adzatembenukira yense kwa anthu ake, nathawira yense kudziko lake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ngati mbawala zosakidwa, ngati nkhosa zopanda wozikusa, munthu aliyense adzabwerera kwa anthu akwawo, aliyense adzathawira ku dziko lake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo padzakhala kuti monga mbawala yothamangitsidwa, ndi monga nkhosa zosazisonkhanitsa anthu, adzatembenukira yense kwa anthu ace, nathawira yense ku dziko lace.