Isaiah 13:19 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Babiloni ufumu wake ndi waulemerero kuposa maufumu ena onse, ndipo anthu ake amaunyadira. Koma Ine Chauta ndidzaononga mzinda wa Babiloniwo monga ndidaonongera Sodomu ndi Gomora pa nthaŵi imene ndidagonjetsa mizindayo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Babiloni, ulemerero wa maufumu, mudzi wokongolawo Ababiloni anaunyadira, adzakhala monga momwe Mulungu anapasula Sodomu ndi Gomora.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Babuloni, ufumu wake ndi waulemerero kuposa mafumu onse. Anthu ake amawunyadira. Koma Yehova adzawuwononga ngati mmene anawonongera Sodomu ndi Gomora.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Babulo, ulemerero wa maufumu, mudzi wokongolawo Akasidi anaunyadira, adzakhala monga momwe Mulungu anapasula Sodomu ndi Gomora.