Isaiah 13:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ine Mulungu mwini wake ndapereka malamulo kwa anthu anga opatulika. Ndasonkhanitsa ankhondo amphamvu, amene amakondwerera kupambana kwanga, kuti akhale zida zanga zolangira amene ndimaŵakwiyira.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ine ndalamulira opatulidwa anga, inde, ndaitana amphamvu anga, achite mkwiyo wanga, okondwerera ndi ukulu wanga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ine Yehova, ndalamulira ankhondo anga; ndasonkhanitsa ankhondo anga kuti akhale zida zanga zolangira amene amadzikuza ndi chipambano changa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ine ndalamulira opatulidwa anga, inde, ndaitana amphamvu anga, acite mkwiyo wanga, okondwerera ndi ukuru wanga.