Isaiah 13:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tamvani phokoso kumapiriku! Likumveka ngati phokoso la chinamtindi cha anthu. Imvani chiwawa m'maufumu! Ndiye ngati mitundu ya anthu ikusonkhana pamodzi. Chauta Wamphamvuzonse akukhazika ankhondo ake mokonzekera kumenya nkhondo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mau a khamu m'mapiri, akunga a mtundu waukulu wa anthu, mau a phokoso la maufumu a mitundu yosonkhanidwa! Yehova wa makamu asonkhanitsa khamu kunkhondo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tamvani phokoso ku mapiri, likumveka ngati phokoso la gulu lalikulu la anthu! Tamvani phokoso pakati pa maufumu, ngati kuti mitundu ya anthu ikusonkhana pamodzi! Yehova Wamphamvuzonse akukhazika asilikali ake mokonzekera kuchita nkhondo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mau a khamu m'mapiri, akunga amtundu waukuru wa anthu, mau a phokoso la maufumu a mitundu yosonkhanidwa! Yehova wa makamu asonkhanitsa khamu kunkhondo.