Isaiah 13:5 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iwowo akuchokera ku maiko akutali, ku malekezero a dziko. Ndiye kuti Chauta wanyamula zida zake zija mokwiya, akubwera kuti adzaononge dziko lonse lapansi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Achokera m'dziko lakutali, kumalekezero a thambo, ngakhale Yehova, ndi zida za mkwiyo wake, kuti aononge dziko lonse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwo akuchokera ku mayiko akutali, kuchokera kumalekezero a dziko Yehova ali ndi zida zake za nkhondo kuti adzawononge dziko la Babuloni.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Acokera m'dziko lakutari, ku malekezero a thambo, ngakhale Yehova, ndi zida za mkwiyo wace, kuti aononge dziko lonse.