Isaiah 13:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Onse adzada nkhaŵa, adzavutika ndi kumva zoŵaŵa, zoŵaŵa zake zonga zimene amazimva mkazi pochira. Azidzayang'anana mwamantha, nkhope zao zidzagwa ndi manyazi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo adzaopa; zowawa ndi masauko zidzawagwira; ndipo adzamva zowawa, ngati mkazi wakubala; adzazizwa wina ndi wina; nkhope zao zidzanga malawi a moto.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthu adzagwidwa ndi mantha aakulu, zowawa ndi masautso zidzawagwera; adzamva zowawa zonga amamva mayi pobereka. Adzayangʼanana mwamantha, nkhope zawo zikufiira ngati malawi amoto.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo adzaopa; zowawa ndi masauko zidzawagwira; ndipo adzamva zowawa, ngati mkazi wakubala; adzazizwa wina ndi wina; nkhope zao zidzanga malawi a moto.