Isaiah 14:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta adzachitira chifundo a m'banja la Yakobe, adzasankhanso Aisraele ndi kuŵalola kuti akhalenso m'dziko lao. Akunja adzabwera kudzakhala nao ndi kuphatikira ku banja la Yakobe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti Ambuye adzamchitira chifundo Yakobo, ndipo adzasankhanso Israele, ndi kuwakhazikitsa m'dziko la kwao; ndipo achilendo adzadziphatika okha kwa iwo, nadzadzigumikiza kunyumba ya Yakobo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova adzachitira chifundo Yakobo; adzasankhanso Israeli ndi kuwalola kuti akhalenso mʼdziko lawo. Alendo adzabwera kudzakhala nawo ndi kudziphatika okha kukhala ngati a mʼnyumba ya Yakobo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti Ambuye adzamcitira cifundo Yakobo, ndipo adzasankhanso Israyeli, ndi kuwakhazikitsa m'dziko la kwao; ndipo acilendo adzadziphatika okha kwa iwo, nadzadzigumikiza ku nyumba ya Yakobo.