Isaiah 14:13 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mumtima mwako unkati, ‘Ndidzakwera mpaka kumwamba. Ndidzakhazika mpando wanga waufumu pamwamba pa nyenyezi za Mulungu. Ndidzakhala pampandopo pa phiri la kumpoto kumene imasonkhanako milungu yonse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo iwe unati mumtima mwako, Ndidzakwera kumwamba, ndidzakweza mpando wanga wachifumu pamwamba pa nyenyezi za Mulungu; ndidzakhala pamwamba pa phiri la khamu, m'malekezero a kumpoto;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mu mtima mwako unkanena kuti, “Ndidzakwera mpaka kumwamba; ndidzakhazika mpando wanga waufumu pamwamba pa nyenyezi za Mulungu; ndidzakhala pa mpando waufumu pa phiri losonkhanirako, pamwamba penipeni pa phiri la kumpoto.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo iwe unati mumtima mwako, Ndidzakwera kumwamba, ndidzakweza mpando wanga wacifumu pamwamba pa nyenyezi za Mulungu; ndidzakhala pamwamba pa phiri la khamu, m'malekezero a kumpoto;