Isaiah 14:19 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma iwe watayidwa kunja kwa manda ako ngati nthambi yoola ndi yonyansa. Mtembo wako waphimbidwa ndi ophedwa amene adabayidwa ndi lupanga, naponyedwa m'dzenje lamiyala. Udzakhala ngati mtembo woponderezedwa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma iwe watayidwa kunja kwa manda ako, ngati nthambi yonyansa, ngati chovala cha ophedwa, opyozedwa ndi lupanga, otsikira kumiyala ya dzenje, monga ngati mtembo wopondedwa ndi phazi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma iwe watayidwa kunja kwa manda ako, ngati nthambi yowola ndi yonyansa. Mtembo wako waphimbidwa ndi anthu ophedwa; amene anabayidwa ndi lupanga, anatsikira mʼdzenje lamiyala ngati mtembo woponderezedwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma iwe watayidwa kunja kwa manda ako, ngati nthambi yonyansa, ngati cobvala ca ophedwa, opyozedwa ndi lupanga, otsikira ku miyala ya dzenje, monga ngati mtembo wopondedwa ndi phazi.