Isaiah 14:2 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu a mitundu ina adzaperekeza Aisraele ku dziko limene Chauta adaŵapatsa. Kumeneko anthuwo adzakhala otumikira Aisraele ngati akapolo ndi adzakazi. Aisraele adzagwira ukapolo anthu amene kale adaali ambuyao ndi kumalamulira anthu amene kale ankaŵazunza.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mitundu ya anthu idzawatenga, ndi kuwafikitsa kumalo a kwao; ndipo a nyumba ya Israele adzakhala nao amitunduwo m'dziko la Yehova, ndi kuwayesa atumiki ndi adzakazi, ndipo amitunduwo adzatengedwa ndende, ndi amenewo anali ndende zao; ndipo Aisraele adzalamulira owavuta.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthu a mitundu ina adzaperekeza a Israeli ku dziko lawo. Tsono Aisraeli adzasandutsa anthu a mitundu ina aja kukhala antchito awo aamuna ndi aakazi mʼdziko la Yehova. Ndiye kuti Aisraeli adzasandutsa akapolo anthu amene kale anali ambuye awo. Iwo adzasandutsa akapolo anthu amene kale ankawalamulira ndi kuwazunza.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mitundu ya anthu idzawatenga, ndi kuwafikitsa ku malo a kwao; ndipo a nyumba ya Israyeli adzakhala nao amitunduwo m'dziko la Yehova, ndi kuwayesa atumiki ndi adzakazi, ndipo amitunduwo adzatengedwa ndende, ndi amenewo anali ndende zao; ndipo Aisrayeli adzalamulira owabvuta.