Isaiah 14:22 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta Wamphamvuzonse akunena kuti, “Ndidzauthira nkhondo mzinda wa Babiloni. Ndidzathetseratu dzina lake ndi onse otsaliramo. Sipadzapulumuka ana ndi zidzukulu zomwe. Ndatero Ine Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Ine ndidzawaukira, ati Yehova wa makamu, ndi kuononga ku Babiloni dzina ndi otsala, ndi mwana wamwamuna, ndi chidzukulu chachimuna, ati Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Ine ndidzathira nkhondo mzinda wa Babuloni. Ndidzachotseratu mu Babuloni dzina lake ndi onse otsaliramo. Ndiye kuti sipadzakhala ana kapena zidzukulu,” akutero Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Ine ndidzawaukira, ati Yehova wa makamu, ndi kuononga ku Babulo dzina ndi otsala, ndi mwana wamwamuna, ndi cidzukulu cacimuna, ati Yehova.