Isaiah 14:25 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Ndidzaŵaononga Aasiriya m'dziko langa, ndipo ndidzaŵapondereza ndi mapazi pa mapiri anga. Tsono anthu anga ndidzaŵavula goli limene Aasiriya adaŵaveka, ndidzaŵachotsera katundu wolemetsa pa mapewa ao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
kuti Ine ndidzathyola Asiriya m'dziko langa, ndi pamwamba pa mapiri anga ndidzawapondereza; pomwepo goli lake lidzachoka pa iwo, ndi katundu wake adzachoka paphuzi pao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndidzawawononga Asiriya mʼdziko langa; ndidzawapondereza ndi mapazi pa mapiri anga; ndidzachotsa goli lawo pa anthu anga, ndipo ndidzachotsa katundu wawo pa mapewa awo.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
kuti Ine ndidzatyola Asuri m'dziko langa, ndi pamwamba pa mapiri anga ndidzawapondereza; pomwepo gori lace lidzacoka pa iwo, ndi katundu wace adzacoka paphuzi pao.