Isaiah 14:29 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Musakondwe inu anthu a ku Filistiya, poona kuti adatha Aasiriya amene adaali ngati ndodo yokumenyani. Mu mtundu wa njoka wamba mudzatuluka mphiri, ndipo mu mtundu wa mphiriyo mudzatuluka chinjoka chaliŵiro chaululu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Usakondwere, iwe Filistiya, wonsewe, pothyoka ndodo inakumenya; pakuti m'muzu wa njoka mudzatuluka mphiri, ndimo chipatso chake chidzakhala njoka yamoto youluka.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Musakondwere inu Afilisti nonse kuti Asiriya amene anali ngati ndodo yokukanthani anathedwa; chifukwa kuchokera ku njoka yomweyi (mfumu ya Aasiriya) mudzatuluka mphiri, ndipo chipatso chake chidzakhala njoka yaliwiro ndiponso yaululu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Usakondwere, lwe Filistia, wonsewe, potyoka ndodo inakumenya; pakuti m'muzu wa njoka mudzaturuka mphiri, ndimo cipatso cace cidzakhala njoka yamoto youluka.