Isaiah 14:30 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Osauka zedi adzapeza chakudya, amphaŵi adzakhala pabwino. Koma mtundu wanu Afilistinu ndidzauwononga ndi njala, ndi otsalira omwe ndidzaŵapha.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndi oyamba kubadwa a osauka adzadya, aumphawi nadzagona pansi osatekeseka; ndipo ndidzapha muzu wako ndi njala, ndi otsala ako adzaphedwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Osaukitsitsa adzapeza chakudya ndipo amphawi adzakhala mwamtendere. Koma anthu ako ndidzawawononga ndi njala, ndipo njalayo idzapha ngakhale opulumuka ako.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndi oyamba kubadwa a osauka adzadya, aumphawi nadzagona pansi osatekeseka; ndipo ndidzapha muzu wako ndi njala, ndi otsala ako adzaphedwa.