Isaiah 14:31 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Lirani kwamphamvu inu apachipata! Pemphani chithandizo mofuula, inu amumzinda! Njenjemerani ndi mantha nonse Afilisti! Onani fumbi likuchita kuti kodoo kuchokera kumpoto, ndipo mwa ankhondo akubwerawo palibe wamantha.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Lira, chipata iwe; fuula, mudzi iwe; wasungunuka, Filistiya wonsewe, pakuti utsi uchokera kumpoto, ndipo palibe wosokera m'mizere yake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Lirani kwambiri, anthu a pa chipata! Fuwulani kwambiri, anthu a mu mzinda! Njenjemerani ndi mantha, inu Afilisti nonse! Mtambo wa utsi ukuchokera kumpoto, ndipo palibe wamantha pakati pa ankhondo ake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Lira, cipata iwe; pfuula, mudzi iwe; wasungunuka, Filistia wonsewe, pakuti utsi ucokera kumpoto, ndipo palibe wosokera m'mizere yace.