Isaiah 14:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Kumanda kwatekeseka kuti kukulandire podzafika iwe mfumu ya ku Babiloni. Mandawo adzutsa mizimu ya anthu akufa kuti ikulonjere iwe, adzutsa mizimu ya onse amene adaali atsogoleri pa dziko lapansi. Akuŵaimiritsa pa mipando yao yaufumu onse amene adaali mafumu a mitundu ya anthu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kunsi kwa manda kugwedezeka, chifukwa cha iwe, kukuchingamira podza pako; kukuutsira iwe mizimu, ngakhale onse akuluakulu a dziko lapansi; kukweza kuchokera m'mipando yao mafumu onse a amitundu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ku manda kwatekeseka kuti akulandire ukamabwera; mizimu ya anthu akufa, aja amene anali atsogoleri a dziko lapansi, yadzutsidwa. Onse amene anali mafumu a mitundu ya anthu ayimiritsidwa pa mipando yawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kunsi kwa manda kugwedezeka, cifukwa ca iwe, kukucingamira podza pako; kukuutsira iwe mizimu, ngakhale onse akuru akuru a dziko lapansi; kukweza kucokera m'mipando yao mafumu onse a amitundu.