Isaiah 15:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nawu ulosi wonena za Mowabu: Chifukwa chakuti mzinda wa Ari waonongedwa usiku umodzi wokha, dziko la Mowabu lagwa. Chifukwa chakuti mzinda wa Kiri waonongedwa usiku umodzi wokha, dziko la Mowabu lagwa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Katundu wa Mowabu. Pakuti usiku umodzi Ari wa ku Mowabu wapasuka, nakhala chabe; usiku umodzi Kiri wa Mowabu wapasuka, nakhala chabe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Uthenga wonena za Mowabu: Popeza kuti mu usiku umodzi wokha mzinda wa Ari wa ku Mowabu wawonongedwa, wawonongedwa pa usiku umodzi wokha. Mzinda wa Kiri wawonongedwa, wawonongedwa pa usiku umodzi wokha.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Katundu wa Moabu. Pakuti usiku umodzi Ara wa ku Moabu wapasuka, nakhala cabe; usiku umodzi Kiri wa Moabu wapasuka, nakhala cabe.