Isaiah 15:2 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu a ku Diboni akukwera ku nyumba ya milungu yao, akukwera ku akachisi ao kukalira. Anthu a ku Mowabu akulira mzinda wa Nebo ndi wa Medeba. Mutu uliwonse wametedwa mpala, ndevu zonse zametedwa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Akwera ku Kachisi, ndi ku Diboni, kumisanje, kukalira; pa Nebo ndi pa Medeba a Mowabu pali kulira; pamitu pao ponse pali dazi, ndevu zonse zametedwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthu a ku Diboni akupita ku nyumba ya milungu yawo, akupita ku malo awo achipembedzo kukalira; anthu a ku Mowabu akulirira mofuwula mzinda wa Nebo ndi wa Medeba. Mutu uliwonse wametedwa mpala, ndipo ndevu zonse zametedwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Akwera kukacisi, ndi ku Dibo, kumisanje, kukalira; pa Nebo ndi pa Medeba a Moabu pali kulira; pamitu pao ponse pali dazi, ndebvu zonse zametedwa.