Isaiah 15:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu a ku Hesiboni ndi ku Eleale akulira mofuula. Mau ao akumveka mpaka ku Yahazi. Nchifukwa chake asilikali a ku Mowabu akulira mofuula, ataya mtima.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndi Hesiboni afuula zolimba, ndi Eleyale; mau ao amveka, ngakhale ku Yahazi; chifukwa chake amuna ankhondo a Mowabu afuula zolimba; moyo wake wanthunthumira m'kati mwake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthu a ku Hesiboni ndi Eleali akulira mofuwula, mawu awo akumveka mpaka ku Yahazi. Kotero asilikali a ku Mowabu akulira mofuwula, ndipo ataya mtima.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndi Hesiboni apfuula zolimba, ndi Eliale; mau ao amveka, ngakhale ku Yahazi; cifukwa cace amuna ankhondo a Moabu apfuula zolimba; moyo wace wanthunthumira m'kati mwace.