Isaiah 15:5 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Inenso ndikulira Mowabu. Anthu ake othaŵa nkhondo akuthaŵira ku Zowari, ku Egilati-Selisiya. Akupita nalira ku chikweza cha Luhiti, akulira mosweka mtima pa mseu wopita ku Horonaimu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mtima wanga ufuula chifukwa cha Mowabu: akulu ake athawira ku Zowari, ku Egilati-Selisiya; pakuti pa chikweza cha Luhiti akwera alikulira, pakuti m'njira ya Horonaimu akweza mfuu wa chionongeko.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Inenso ndikulirira Mowabu; chifukwa othawa nkhondo ake akupita akulira ku chikweza cha Luluti mpaka ku Zowari ndi Egilati-Selisiya akupita akulira ku chikweza cha Luhiti, Akulira mosweka mtima pa njira yopita ku Horonaimu; akulira mosweka mtima chifukwa cha chiwonongeko chawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mtima wanga upfuula cifukwa ca Moabu: akuru ace athawira ku Zoari, ku Eglatiselisiya; pakuti pa cikweza ca Luhiti akwera alikulira, pakuti m'njira ya Horanaimu akweza mpfuu wa cionongeko.