Isaiah 15:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Madzi a ku Diboni asakanizika ndi magazi, komabe ndidzafikitsa zovuta zina zambiri pa Diboni. Ndidzafikitsa mkango woti udzagwire aliyense wopulumuka ku Mowabu, ndiponso aliyense wotsalira m'dzikomo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti madzi a Diboni adzala mwazi; pakuti ndidzatengera zina pa Diboni, mkango pa iye amene anapulumuka ku Mowabu, ndi pa otsala a m'dziko.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Madzi a ku Dimoni afiira ndi magazi, komabe ndidzabweretsa zina zambiri pa Dimoni, mkango woti udzagwire aliyense othawa mu Mowabu ndi aliyense wotsala mʼdzikomo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti madzi a Dimoni adzala mwazi; pakuti ndidzatengera zina pa! Dimoni, mkango pa iye amene anapulumuka ku Moabu, ndi pa otsala am'dziko.