Isaiah 16:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Amowabu atumiza mphatso ya mwanawankhosa kwa wolamulira dziko. Iwo achokera ku mzinda wa Sela, adzera njira ya chipululu mpaka kukafika ku phiri la Ziyoni.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Tumizani inu anaankhosa kwa wolamulira wa dziko kuchokera ku Sela kunka kuchipululu, mpaka kuphiri la mwana wamkazi wa Ziyoni.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthu a ku Mowabu atumiza mphatso za ana ankhosa onenepa, kuchokera ku Sela kudutsa chipululu mpaka kukafika ku phiri la Ziyoni.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Tumizani inu ana a nkhosa kwa wolamulira wa dziko kucokera ku Sela kunka kucipululu, mpaka ku phiri la mwana wamkazi wa Ziyoni.