Isaiah 16:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kukondwa ndi kusangalala kwalekeka ku minda yadzinthu. Nyimbo sizikuimbidwa, palibenso kufuula m'minda yamphesa. Palibe wopsinya vinyo mopondera mphesa, kufuula kwachimwemwe kwa nthaŵi yotchera mphesa kwalekeka.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo chikondwero ndi msangalalo zachotsedwa m'munda wopatsa zipatso; ndi m'minda ya mipesa simudzakhala kuimba, ngakhale phokoso losangalala; palibe woponda adzaponda vinyo m'moponderamo; ndaleketsa mfuu wa masika amphesa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chimwemwe ndi chisangalalo zalekeka ku minda yanu ya zipatso; palibe amene akuyimba kapena kufuwula mʼminda ya mpesa; palibe amene akupsinya vinyo ku malo opsinyira mphesa, pakuti ndathetsa kufuwula.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo cikondwero ndi msangalalo zacotsedwa m'munda wapatsa zipatso; ndi m'minda ya mipesa simudzakhala kuyimba, ngakhale phokoso losangalala; palibe woponda adzaponda vinyo m'moponderamo; ndaleketsa mpfuu wa masika amphesa.