Isaiah 16:12 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ngakhale Amowabu akudzipereka pakupita ku akachisi ao namakapemphera mpaka kutopa, zimenezo sizidzaŵapindulira kanthu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo padzakhala kuti pamene Mowabu adzadzionetsa yekha, ndi kudzitopetsa pamsanje, ndipo kufika kumalo ake oyera kudzapemphera, sadzapindulapo kanthu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ngakhale anthu a ku Mowabu apite ku malo awo achipembedzo koma amangodzitopetsa ndi kutaya nthawi chabe chifukwa sizidzatheka.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo padzakhala kuti pamene Moabu adzadzionetsa yekha, ndi kudzitopetsa pamsanje, ndipo kufika ku malo ace oyera kudzapemphera, sadzapindulapo kanthu.