Isaiah 16:14 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma tsopano akunena kuti, “Zisanathe zaka zitatu, potsata m'mene amaŵerengera munthu waganyu, ulemerero wa Mowabu udzakhala utatheratu. Chigulu chachikulu cha anthu ake chidzaonongeka, ndipo opulumukapo adzakhala ochepa ndi ofooka.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma tsopano Yehova wanena, nati, Zisanapite zaka zitatu monga zaka za wolembedwa ntchito, ulemerero wa Mowabu udzakhala wonyozeka, ndi khamu lalikulu lake, ndi otsala adzakhala ang'onong'ono ndi achabe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma tsopano Yehova akuti, “Zisanathe zaka zitatu, potsata mʼmene munthu waganyu amawerengera, ulemerero wa Mowabu udzakhala utatheratu ndipo anthu ake ambiri adzakhala atawonongeka, ndipo opulumuka ake adzakhala ochepa ndi ofowoka.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma tsopano Yehova wanena, nati, Zisanapite zaka zitatu monga zaka za wolembedwa nchito, ulemerero wa Moabu udzakhala wonyozeka, ndi khamu lalikuru lace, ndi otsala adzakhala ang'ongong'ono ndi acabe.