Isaiah 16:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Akuuza anthu a ku Yuda kuti, “Mutiwuze chochita, gamulani zoti tichite. Pamene dzuŵa lili pa liwombo, mutipatse mthunzi wabii ngati mdima. Mutibise ife anthu opirikitsidwa, musatipereke ife anthu othaŵa nkhondo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chitani uphungu, weruzani chiweruziro; yesa mthunzi wako monga usiku pakati pa usana; bisa opirikitsidwa, osawulula woyendayenda.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Amowabu aja anawuza a ku Yuda kuti, “Tiwuzeni chochita, gamulani zoti tichite. Inu mutiteteze kwa adani anthu. Mukhale ngati mthunzi wathu dzuwa lili pa liwombo. Mutibise, musatipereke ife othawa nkhondo kwa adani athu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Citani uphungu, weruzani ciweruziro; yesa mthunzi wako monga usiku pakati pa usana; bisa opitikitsidwa, osaulula woyendayenda.