Isaiah 16:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Othaŵa nkhondo a ku Mowabu azikhala pakati panu. Mukhale populumukira pao kwa woononga uja.” Nthaŵi ikudza pamene kupsinja sikudzakhalaponso, kuwononga kudzaleka, ndipo amene amaŵapondereza adzachoka m'dzikomo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Opirikitsidwa a Mowabu akhale ndi iwe, khala iwe chomphimba pamaso pa wofunkha; pakuti kumpambapamba kwalekeka, kufunkha kwatha, opondereza atsirizika m'dziko.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Lolani kuti anthu othawa nkhondo a ku Mowabu azikhala pakati panu; mukhale populumukira pawo kwa wowonongayo.” Nthawi idzafika ndipo wozunzayo sadzakhalaponso, kuwononga kudzaleka; waukaliyo adzachoka mʼdzikomo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Opitikitsidwa a Moabu akhale ndi iwe, khala iwe comphimba pamaso pa wofunkha; pakuti kumpambapamba kwalekeka, kufunkha kwatha, opondereza atsirizika m'dziko.