Isaiah 16:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu a ku Yuda akunena kuti, “Kudzikuza kwa Amowabu takumva, adadzikuza kwambiri. Kudzitukumula kwao, kunyada kwao, kunyodola kwao ndi kudzitama kwao, zonse nzachabechabe.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ife tinamva kunyada kwa Mowabu, kuti iye ali wonyada ndithu; ngakhale kudzitama kwake, ndi kunyada kwake ndi mkwiyo wake; matukutuku ake ali achabe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tinamva kuti Mowabu anadzikuza kwambiri. Kunyada kwawo ndi kunyogodola kwawo ndi kudzitama kwawo, zonse ndi zopanda phindu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ife tinamva kunyada kwa Moabu, kuti iye ali wonyada ndithu; ngakhale kudzitama kwace, ndi kunyada kwace ndi mkwiyo wace; matukutuku ace ali acabe.